Çiçevaca Meal — Hâlid İbrahim Batyala — Mâûn 107:1 – Nas 114:6
Contents
- Mâûn 107:1
- Mâûn 107:2
- Mâûn 107:3
- Mâûn 107:4
- Mâûn 107:5
- Mâûn 107:6
- Mâûn 107:7
- Kevser 108:1
- Kevser 108:2
- Kevser 108:3
- Kâfirun 109:1
- Kâfirun 109:2
- Kâfirun 109:3
- Kâfirun 109:4
- Kâfirun 109:5
- Kâfirun 109:6
- Nasr 110:1
- Nasr 110:2
- Nasr 110:3
- Tebbet 111:1
- Tebbet 111:2
- Tebbet 111:3
- Tebbet 111:4
- Tebbet 111:5
- İhlas 112:1
- İhlas 112:2
- İhlas 112:3
- İhlas 112:4
- Felak 113:1
- Felak 113:2
- Felak 113:3
- Felak 113:4
- Felak 113:5
- Nas 114:1
- Nas 114:2
- Nas 114:3
- Nas 114:4
- Nas 114:5
- Nas 114:6
Mâûn 107:1
Kodi wamuona yemwe akutsutsa za mphoto (ndi chiwerengero cha tsiku lachimaliziro)?[487]
———
[487] Sura imeneyi ikufotokoza m’mene alili makhalidwe a anthu ambiri, ngakhale amene amadzitcha kuti ndi Asilamu. Aliyense amene ali ndi makhalidwe otere ndiye kuti sakhulupilira za tsiku la chiweruziro. Akadakhala kuti akukhulupilira za tsikuli, sibwenzi akusiya kuwachitira za chifundo osauka ndi amasiye. Sapereka chithandizo ngakhale kulimbikitsa ena ngati iye alibe.
Mâûn 107:2
Iye ndi yemwe akukankha wamasiye (mwankhanza).
Mâûn 107:3
Ndipo salimbikitsa (ena pamodzi ndi iye mwini) kudyetsa osauka.
Mâûn 107:4
Choncho kuonongeka kuli pa ena mwa opemphera swala (amene ali ndi mbiri izi);
Mâûn 107:5
Omwe amachitira mphwayi mapemphero awo.[488]
———
[488] Kuchitira mphwayi mapemphero (Swala), kumeneku ndiko kupemphera modukizadukiza. Tsiku lina nkupempherapo, tsiku lina ayi. Kapenanso kupemphera modzionetsera kwa anthu (riyaa).
Mâûn 107:6
Amenenso (akamachita mapemphero awo) amadzionetsera (kwa anthu mwachipha maso kuti apeze ulemelero ndi kutamandidwa mmitima mwa anthu).[489]
———
[489] Riyaa ndiko kuchita ntchito yabwino ndicholinga choonetsa anthu, kuti akuone kuti ndiwe wabwino, mwina kuti ukhale wokondedwa ndi anthu. Kapenanso kuti upeze za m’matumba mwawo. Amenewa ndi machitidwe a “Shiriki” (kum’phatikiza Allah ndi zolengedwa Zake pa mapemphero) ndiponso ndi njira yobera anthu.
Mâûn 107:7
Ndipo amamana ziwiya (zawo posabwereka anzawo zinthu zofunika pa moyo wa aliyense monga nkhwangwa, mpeni, mtondo ndi zina zotere).
Kevser 108:1
Ndithu takupatsa zabwino zambiri (zina mwa izo ndi mtsinje wotchedwa Kauthar).[490]
———
[490] Tanthauzo la “zabwino zambiri” apa, ndi uneneri, maphunziro, ntchito zabwino, ulemelero, kupambana pakukhala ndi omutsatira ambiri ndi zabwino zina zam’dziko lino lapansi ndi tsiku lachimaliziro, zosawerengeka zomwe sadapatsidwe aliyense pambuyo pa iye ngakhale mtsogolo mwake. Ndithu zimenezi, popanda chikaiko, ndizabwino kwambiri kuposa chuma ndi ana.
Kevser 108:2
(Pakuti ndakupatsa zimenezo), pitiriza kupembedza Mbuye wako (moyera mtima) ndipo ipha nsembe yako (chifukwa chakuthokoza Allah pa zimene wakupatsa, monga ulemelero ndikukusankhira zabwino zambiri).[491]
———
[491] Tanthauzo loti “Mbuye wako yekha umupembedze” nkuti amupembedze Allah Yekha, asachite chiphamaso, asakhale monga amene amachita mapemphero ndi cholinga choti adzionetsere kwa anthu. Ndikutinso apereke nsembe m’dzina Lake, osati azimu ndi zina zotero.
Kevser 108:3
Ndithu mdani wako ndiye ali wopanda mwawi. [492]
———
[492] Adani a Mtumiki (s.a.w) adali kukondwera kwambiri pamene ankaona kuti ana ake onse achimuna atha kumwalira, iwo ankaona kuti palibe ubwino uli onse kwa munthu pano pa dziko ngati sadapatsidwe ana achimuna ndi chuma. Pa chifukwa ichi, adali kumutcha “Abtar,” wopanda madalitso. Msura imeneyi Allah akumtonthoza Mneneriyo ndiponso akuyankha adani ake.
Kâfirun 109:1
Nena (iwe Mtumiki) (s.a.w): E inu anthu osakhulupirira![493]
———
[493] (Ndime 1-6) Osakhulupilira a mu mzinda wa Makka pamene adaona kuti atopa, sangathe kuzimitsa dangalira la Usilamu ndipo adamuona Mneneri (s.a.w) tsiku lililonse akuonjezera khama pa ntchito yake, chipembedzo nacho chikunkerankera mtsogolo, adapempha Muhammad (s.a.w) kuti pakhale chimvano pakati pa iwo ndi iye choti amupembedze Mulungu wa Mneneri (s.a.w) chaka chimodzi pamodzi naye, nayenso pa chaka chinacho asakanikirane nawo popembedza milungu yawo chaka chimodzinso. Kumeneku ndiko kuti chaka, apembedze Mulungu wa Mneneri (s.a.w), nayenso apembedze milungu yawo chaka chinacho. Apa ndipo pamene idavumbulutsidwa Surayi. Cholinga chake ndi ichi: Inu muli ndi milungu yanu, inenso ndili ndi Mulungu wanga. Sizingatheke kusakanikirana pakati pa milungu yanu yonama ndi Mulungu wanga woona, ngakhalenso ndi mapemphero anu onama ndi mapemphero anga owona. Inu muli ndi chipembedzo ndichikhulupiliro chanu, inenso ndili ndi chipembedzo ndi chikhulupiliro changa.
Kâfirun 109:2
Sindipembedza chimene inu mukuchipembedza (kusiya Allah).
Kâfirun 109:3
Inunso simumpembedza amene ine ndikumpembedza (yemwe ndi Allah).
Kâfirun 109:4
Ndiponso ine sindidzapembedza chimene inu mwakhala mukuchipembedza (chifukwa inu ndinu ophatikiza Allah ndi zinthu zina).
Kâfirun 109:5
Ndipo inu simudzampembedza amene ine ndikumpembedza (yemwe ndi Allah).
Kâfirun 109:6
Inu muli ndi chipembedzo chanu (chimene mukuchikhulupirira), inenso ndili ndi chipembedzo changa (chimene Allah wandisankhira).
Nasr 110:1
Chikafika chipulumutso cha Allah ndi kugonjetsa (mzinda wa Makka kwa iwe ndi okutsatira),[494]
———
[494] Ili ndi lonjezo la Allah kwa Mneneri wake (Muhammad) (s.a.w) kuti amthandiza kumpulumutsa kwa adani ake amene adali kumuzunza ndi kufuna kumupha. Lonjezoli lidali lakuti iye adzaulamulira mzinda wa adaniwo momwe adamutulutsa.
Nasr 110:2
Ndikuwaona anthu akulowa m’chipembedzo cha Allah ali magulumagulu,[495]
———
[495] Mneneri (s.a.w) pamene adalowa mu mzinda wa Makka ndi kugonjetsa adani ake monga momwe Allah adamulonjezera, a kafiri adali kubwera m’mafukomafuko kudzalowa m’chipembedzo cha Chisilamu.
Nasr 110:3
Pamenepo lemekeza Mbuye wako ndi kumtamanda ndiponso mpemphe chikhululuko, ndipo ndithu Iye ndiwolandira mochuluka kulapa (kwa anthu Ake).[496]
———
[496] Tanthauzo la kuuzidwa Mneneri Muhammad (s.a.w) kuti zikachitika zimene adalonjezedwa, amulemekeze Mbuye wake, amupemphe chikhululuko, chikhalirecho iye adali kuchita zimenezo, izi zimatanthauza kuti moyo wake wayandikira kutha, watsala pang’ono kumwalira. Choncho adalamulidwa kuonjezera mapemphero kuti aonjezere kulinganiza tsiku lake lomaliza. Imeneyi ndi imodzi mwa Surah zimene zidavumbulutsidwa kotsirizira kwa moyo wa Mtumiki (s.a.w). Pamene idavumbulutsidwa Surayi, ena mwa maswahaba (omutsatira) adazindikira chinsinsi cha Surayi; adali kulira poona kuti Mneneri (s.a.w) amwalira posachedwa. Pambuyo povumbulutsidwa Surayi, Mneneri (s.a.w) sadakhale moyo nthawi yaitali.
Tebbet 111:1
Aonongeka manja a Abi Lahab (omwe adali kuwagwiritsa ntchito pozunza Asilamu). Nayenso wawonongeka.[497]
———
[497] (Ndime 1-4) Pa chiyambi cha uneneri wa Muhammad (s.a.w) adalamulidwa kuti aulalikire uthenga wabwinowo kwa abale ake apafupi; adawasonkhanitsa ndipo adawalalikira ndi kuwachenjeza za chilango cha tsiku lachimaliziro. Koma Abu Lahab adali m’bale watate wa Mtumiki Muhammad (s.a.w) adakwiya ndipo adanena kuti: “Waonongeka iwe! Waonongeka iwe! Chimenechi ndi chimene watisonkhanitsira?’’ Pa chifukwa ichi idavumbulutsidwa Sura imeneyi. Allah adamubwezera Abu Lahab pamodzi ndi mkazi wake, Ummu Jamil, mawu otembelera. Ummu Jamil ankalimbikira kwambiri kumuzunza Mtumiki (s.a.w) ndi kuwakaikitsa amuna kuti asamutsatire. Ndipo adayesetsa kutsekereza kuti asamutsatire. Ndipo adayesetsa kutsekereza kuti Chisilamu chisafalikire madera ena. “Aonongeka manja a Abu Lahab’’ kumeneku ndi kutembelera komutembelera Abu Lahab kuti aonongeke m’malo moonongeka Mneneri (s.a.w). Pakuti amene amatembelera apayu ndi Mwini Allah, ndiye kuti matembelero adamufikiradi iye.
Tebbet 111:2
Chuma chake ndi ulemelero wake (umene adaupeza) sizidamthandize ku chilango cha Allah.
Tebbet 111:3
Adzalowa ku Moto wa malawi.
Tebbet 111:4
Nayenso mkazi wake (adzalowa ku Moto) yemwe adali kusenza nkhuni (za minga pomutchera Mtumiki (s.a.w) komanso amanka nadanitsa pakati pa anthu).
Tebbet 111:5
Mkhosi mwake mdzamangidwa chingwe chopiringidwa bwino cha mlaza (chomlanga nacho).[498]
———
[498] Uyu mkazi wa Abu Lahab adali wodanitsa. Ntchito yake idali kutapa mawu uku, kuwapititsa uku, ncholinga chofuna kusokoneza.
İhlas 112:1
Nena (iwe Mtumiki (s.a.w), kwa amene akukufunsa mwachipongwe, mbiri za Mulungu wako): “Iye ndi Allah Mmodzi, (alibe mnzake).
İhlas 112:2
Allah ndi Wokhala ndi zonse Wodaliridwa ndi zolengedwa Zake.
İhlas 112:3
Sadabale (mwana) ndiponso sadaberekedwe.
İhlas 112:4
Ndiponso palibe aliyense wofanana ndi Iye.”
Felak 113:1
Nena: “Ndikudzitchinjiriza ndi Mbuye wam’bandakucha.[499]
———
[499] Surayi ndi yotsatirayi, zidavumbulutsidwa nthawi imodzi. Koma pali kutsutsana; ena akuti zidavumbulutsidwa ku Makka pomwe ena akuti zidavumbulutsidwa ku Madina. Sura ziwirizi zikutiphunzitsa m’mene tingadziikire mchitetezo cha Allah, ndiponso tikuphunzitsidwa kuti Iye (Allah) ndi mwini mphamvu zonse. Atha kumuteteza munthu kuchinthu chilichonse chifukwa chakuti Iye (Allah) ndi Mlengi wa chinthu chilichonse. Choncho, yemwe asiya chitetezo Chake ndikumafuna chitetezo cha ufiti, azimu, manda, ndi zina zotero ndiye kuti akuziika iye mwini kumachitidwe a “SHIRIK” (kupembedza mafano).
Felak 113:2
Kuchokera ku zoipa zimene Iye adazilenga.[500]
———
[500] “Zomwe adalenga” zikutanthauza chilichonse cholengedwa, chamoyo ndi chopanda moyo; chooneka ndi chosaoneka.
Felak 113:3
Ndi ku zoipa za usiku pamene mdima ukulowa mwa mphamvu.[501]
———
[501] Palibe chikaiko, usiku wa mdima uli ndi zoopsa zambiri zomwe sizipezeka masana ndi usiku wowala. Mu usiku wa mdima, mumayenda zinthu zoopsa zambiri, monga zirombo zolusa, akuba, achiwembu ndi zina zambiri. Kukacha zonsezi zimabisala koma kukada zimatuluka.
Felak 113:4
Ndi ku zoipa za afiti omwe amauzira mu mfundo.
Felak 113:5
Ndiponso ku zoipa za wansanje pamene akuchita nsanje.”[502]
———
[502] “Wanjiru” kapena “Wansanje” uyu ndi munthu amene amanyansidwa akamuona mnzake atadalitsidwa ndi dalitso la mtundu uliwonse. Ndipo amakhumba kuti dalitsolo limuchokere ngakhale kuti lisamufikire iye. Njiru ndi tchimo lalikulu ndiponso ndi nthenda yoipa kwambiri. Mwina munthu wanjiru amabisa njiru yake mu mtima mpaka kufa nayo. Apo amapuma iye pamodzi ndi anthu aja amene ankawachitira njiru. Mwina amalephera kuibisa mu mtima ndipo amaionetsera poyera kotero kuti amachita zotheka kuti amuchotsere mnzake uja dalitso lomwe wapatsidwa ndi Allah. Akalephera izi, amangoganiza za kumupha; njiru iyi ndi yoipa kwambiri.
Nas 114:1
Nena: “Ndikudzitchinjiriza ndi Mbuye (Mleri) wa anthu (Yemwe akulinganiza zinthu zawo).[503]
———
[503] Allah pokhala Mlengi wa anthu ndi amenenso amawalera kuyambira pamene ali m’mimba mpaka kumapeto a moyo wawo pano pa dziko. Kuwaleraku kuli muuzimu, mthupi, mu mpweya, ndi pa chilichonse chofunika pa moyo wawo. Kuonjezera pa zimenezi adawapatsa nzeru ndi kuwasonyeza njira zabwino za dziko lapansi ndi tsiku lachimaliziro. Ndipo adawalamula kuzitsata njirazo. Adawasonyezanso njira zoipa za dziko lino lapansi ndi tsiku lachimaliziro. Ndipo adawalamula kuti azipewe njira zoipazo.
Nas 114:2
Mfumu ya anthu ( Imene iri ndi mphamvu yochita chirichonse pa iwo).
Nas 114:3
Wopembedzedwa wa anthu.
Nas 114:4
Kuzoipa za mnong’onezi (yemwe amathira unong’onezi wake m’mitimaya anthu) yemwenso amabisala (posiya unong’onezi wake ngati mwini mtimawo atankumbukira Allah).[504]
———
[504] Mnong’onezi wa zoipa amene amabisala ndiye Satana, yemwe ntchito yake ndi kunong’oneza zoipa m’mitima ya anthu pofuna kuwasokeretsa ndi kuwaiwalitsa Allah. Koma akakumana ndi munthu wa chikhulupiliro cha mphamvu kapena yemwe amatamanda kwambiri Mbuye wake Allah, Satanayo amalephera ndipo amathawa; kubwerera m’mbuyo.
Nas 114:5
Yemwe amanong’oneza mzifuwa za anthu.
Nas 114:6
Wochokera m’ziwanda ndi mwa anthu.”[505]
———
[505] Mchiyankhulo cha Chiarabu aliyense woipitsitsa amatchedwa “shaitan” satana, munthu kapena chiwanda. Satana wa muwanthu ndiwoipitsitsa kwambiri kwa anthu kuposa wa m’ziwanda.